15 omangira malamba m'cuuno mwao, ndi nduwira zazikuru zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babulo, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi.
16 Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga ku dziko la Akasidi.
17 Namdzera a ku Babulo ku kama wa cikondi, namdetsa ndi cigololo cao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wace unafukidwa nao.
18 M'mwemo iye anaulula cigololo cace, nabvula umarisece wace; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkuru wace.
19 Koma anacurukitsa zigololo zace, nakumbukila masiku a ubwana wace, muja anacita cigololo m'dziko la Aigupto.
20 Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya aburu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.
21 Momwemo wautsanso coipa ca ubwana wako, pakukhudza Aaigupto nsonga za maere ako, cifukwa ca maere a ubwana wako.