18 M'mwemo iye anaulula cigololo cace, nabvula umarisece wace; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkuru wace.
19 Koma anacurukitsa zigololo zace, nakumbukila masiku a ubwana wace, muja anacita cigololo m'dziko la Aigupto.
20 Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya aburu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo.
21 Momwemo wautsanso coipa ca ubwana wako, pakukhudza Aaigupto nsonga za maere ako, cifukwa ca maere a ubwana wako.
22 Cifukwa cace, Oholiba, atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakuutsira mabwenzi ako amene moyo wako wakufidwa nao, ndi kukufikitsira iwowa pozungulira ponse atsutsane nawe,
23 a ku Babulo, ndi Akasidi, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasuri onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo.
24 Ndipo adzakudzera ndi zida, magareta a nkhondo, ndi magareta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zocinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao.