22 Amalonda a ku Seba ndi a ku Rama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa ziri zonse, ndi miyala iri yonse ya mtengo wace, ndi golidi.
23 Harani ndi Kane ndi Edene, amalonda a ku Seba Asuri ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda.
24 Awa anagulana nawe malonda ndi zobvala zosankhika, ndi mitumba ya nsaru zofiirira ndi zopikapika, ndi cuma ca thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako.
25 Zombo za ku Tarisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzazidwa ndi cuma ndi ulemu waukuru pakati pa nyanja,
26 Opalasa ako anakufikitsa ku madzi akuru; mphepo ya kum'mawa inakutyola m'kati mwa nyanja,
27 Cuma cako, zako zogulana nazo malonda ako, amarinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.
28 Pakumveka mpfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka.