25 Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zirombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'cipululu, ndi kugona kunkhalango.
26 Pakuti ndidzaika izi ndi miraga yozungulira citunda canga; zikhale mdalitso; ndipo ndidzabvumbitsa mibvumbi m'nyengo yace, padzakhala mibvumbi ya madalitso.
27 Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zace, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa.
28 Ndipo sadzakhalanso cakudya ca amitundu, ndi cirombo ca kuthengo sicidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.
29 Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzacotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.
30 Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndiri nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israyeli, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.
31 Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa za pabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.