3 Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ace ngati amkuwa, ndi cingwe cabwazi m'dzanja lace, ndi bango loyesa nalo, naima kucipata iye.
4 Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israyeli zonse uziona.
5 Ndipo taonani, panali linga kunja kwace kwa nyumba ya kacisi poizinga, ndi m'dzanja lace la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uli wonse mkono kudza cikhato; ndipo anayesa cimangidweco kucindikira kwace bango limodzi, ndi msinkhu wace bango limodzi.
6 Pamenepo anafika ku cipata coloza kum'mawa, nakwera pa makwerero ace; ndipo anayesa ciundo ca cipata, bango limodzi kucindikira kwace; ndico ciundo coyamba, bango limodzi.
7 Ndi cipinda ca alonda, conse nca bango limodzi m'litali mwace, ndi bango limodzi kupingasa kwace, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi ciundo ca cipata ku mbali ya ku khonde la kucipata m'katimo, bango limodzi.
8 Anayesanso khonde la kucipata ku mbali ya kukacisi, bango limodzi.
9 Pamenepo anayesa khonde la kucipata mikono isanu ndi itatu, ndi mphuthu zace mikono iwiri; ndi khonde la kucipata linaloza kukacisi.