1 Ndipo kunali caka cacisanu ndi cimodzi, mwezi wacisanu ndi cimodzi, tsiku lacisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.
2 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, cifaniziro ca maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace, moto; ndi kuyambira m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace, monga maonekedwe a ceza, ngan citsulo cakupsa.
3 Ndipo anatambasula conga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku citseko ca cipata ca bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje locititsa nsanje.
4 Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa lsrayeli, monga mwa maonekedwe ndinawaona ku cidikha cija.