3 ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisrayeli: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili,
4 limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, m'ng'anjo ya citsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwacita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;
5 kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko mayenda mkaka ndi uci, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.
6 Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwacita.
7 Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawaturutsa iwo ku dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.
8 Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.
9 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ciwembu caoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu.