1 Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'cuuno mwako, usauike m'madzi.
2 Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kubvala m'cuuno mwanga.
3 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti,
4 Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'cuuno mwako, nuuke, nupite ku Firate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.
5 Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Firate, monga Yehova anandiuza ine.
6 Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Firate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.
7 Ndipo ndinanka ku Firate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu.