1 Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za cirala.
2 Yuda alira, ndipo zipata zace zilefuka, zikhala pansi zobvekedwa ndi zakuda; mpfuu wa Yerusalemu wakwera.
3 Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.
4 Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.
5 Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.
6 Mbidzi zinaima pamapiri oti se, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, cifukwa palibe maudzu.