10 Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Cifukwa cace nciani kuti Yehova watinenera ife coipa cacikuru ici? mphulupulu yathu ndi yanji? cimo lathu lanji limene tacimwira Yehova Mulungu wathu?
11 Pamenepo uziti kwa iwo, Cifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu yina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga cilamulo canga;
12 ndipo mwacita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wace woipa, kuti musandimvere Ine;
13 cifukwa cace ndidzakuturutsani inu m'dziko muno munke ku dziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu yina usana ndi usiku, kumene sindidzacitira inu cifundo.
14 Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto.
15 Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kucokera ku dziko la kumpoto, ndi ku maiko ena kumene anawapitikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso ku dziko lao limene ndinapatsa makolo ao.
16 Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pace ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.