11 Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsya; cifukwa cace ondisautsa adzapunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, cifukwa sanacita canzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.
12 Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona imso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera cilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.
13 Muyimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ocita zoipa.
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine.
15 Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.
16 Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mpfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;
17 cifukwa sanandipha ine m'mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yace yaikuru nthawi zonse.