3 Ndipo panali m'mawa mwace, kuti Pasuri anaturutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanacha dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.
4 Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe coopsa ca kwa iwe mwini, ndi kwa abale ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babulo, nadzawapha ndi lupanga,
5 Ndiponso ndidzapereka cuma conse ca mudzi uwu, ndi zaphindu zace zonse, ndi zinthu zace zonse za mtengo wace, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babulo.
6 Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babulo, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza.
7 Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala coseketsa dzuwa lonse, lonse andiseka.
8 Pakuti pali ponse ndinena, ndipfuula; ndipfuula, Ciwawa ndi cofunkha; pakuti mau a Mulungu ayesedwa kwa ine citonzo, ndi coseketsa, dzuwa lonse.
9 Ndipo ngati nditi, Sindidzamchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lace, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.