6 Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Gileadi, ndi mutu wa Lebano; koma ndidzakuyesa iwe cipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.
7 Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zace; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.
8 Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzace, Yehova anatero nao mudzi waukuru uwu cifukwa ninji?
9 Ndipo adza yankha, Cifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu yina, ndi kuitumikira.
10 Musamlirire wakufa, musacite maliro ace; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.
11 Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwace mwa Yosiya atate wace, amene anaturuka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iri yonse;
12 koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili.