1 Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! ati Yehova.
2 Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipitikitsa, ndipo simunazizonda; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa nchito zanu, ati Yehova.
3 Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipitikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso ku makola ao; ndipo zidzabalana ndi kucuruka.
4 Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.
5 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzacita mwanzeru, nadzacita ciweruzo ndi cilungamo m'dziko lino.
6 Masiku ace Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israyeli adzakhala mokhazikika, dzina lace adzachedwa nalo, ndilo Yehova ndiye cilungamo cathu.