4 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babulo:
5 Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zace;
6 tengani akazi, balani ana amuna ndi akazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana amuna ndi akazi; kuti mubalane pamenepo, musacepe.
7 Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wace inunso mudzakhala ndi mtendere.
8 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
9 Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.
10 Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babulo, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakucitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.