3 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisrayeli ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera ku dziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.
4 Awa ndi mau ananena Yehova za Israyeli ndi Yuda.
5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.
6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; cifukwa canji ndiona mwamuna ndi manja ace pa cuuno cace, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
7 Kalanga ine! pakuti nlalikuru tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.
8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;
9 koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene ndidzawaukitsira.