4 Awa ndi mau ananena Yehova za Israyeli ndi Yuda.
5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.
6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; cifukwa canji ndiona mwamuna ndi manja ace pa cuuno cace, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
7 Kalanga ine! pakuti nlalikuru tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.
8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;
9 koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene ndidzawaukitsira.
10 Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israyeli; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutari, ndi mbeu zako ku dziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala cete, palibe amene adzamuopsya.