27 Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu lonse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?
28 Cifukwa cace Yehova atero: Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la Akasidi, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzaulanda,
29 ndipo Akasidi, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa macitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu yina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.
30 Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Yuda anacita zoipa zokha zokha pamaso panga ciyambire ubwana wao, pakuti ana a Israyeli anandiputa Ine kokha kokha ndi nchito ya manja ao, ati Yehova.
31 Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiucotse pamaso panga;
32 cifukwa ca zoipa zonse za ana a Israyeli ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.
33 Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvera kulangizidwa.