1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,
2 Pita ku nyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'cipinda cina, nuwapatse iwo vinyo amwe.
3 Ndipo ndinatenga Yaasaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habazinya, ndi abale ace, ndi ana amuna ace, ndi nyumba yonse ya Arekabu;
4 ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, cokhala pambali pa cipinda ca akuru, ndico cosanjika pa cipinda ca Maseya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;
5 ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.
6 Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya;
7 ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.