16 Ndipo Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.
17 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ngati mudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;
18 koma ngati simudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Akasidi, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.
19 Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Akasidi, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.
20 Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, comweco kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.
21 Koma ngati mukana kuturuka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa:
22 Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzaturutsidwa kunka kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.