14 iwonso anatumiza, namcotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.
15 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m'bwalo la kaidi, kuti,
16 Pita, ukanene kwa Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osaucitira zabwino; ndipo adzacitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.
17 Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.
18 Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati cofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.