18 Njira yako ndi nchito zako zinakucitira izi; ici ndico coipa cako ndithu; ciri cowawa ndithu, cifikira ku mtima wako.
19 Matumbo anga, matumbo anga! ndipoteka pamtima panga peni peni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.
20 Alalikira cipasuko cilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsaru zanga zocinga m'kamphindi.
21 Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga?
22 Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ocenjera kucita coipa koma kucita cabwino sakudziwa.
23 Ndinaona dziko lapansi, ndi rpo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika.
24 Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka.