14 ndi kuti, Iai; tidzanka ku Aigupto, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;
15 cifukwa cace mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Aigupto, kukakhala m'menemo;
16 pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Aigupto, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Aigupto; pamenepo mudzafa.
17 Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.
18 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.
19 Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Aigupto; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.
20 Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.