7 Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya.
8 Ndipo anaitana Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru,
9 nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pace,
10 Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa naco cisoni coipa cimene ndakucitirani inu.
11 Musaope mfumu ya ku Babulo, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndiri ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lace.
12 Ndipo ndidzakucitirani inu cifundo, li kuti iye akucitireni inu cifundo, nakubwezereni inu ku dziko lanu.
13 Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;