2 Za Aigupto: kunena za nkhondo ya Farao-neko mfumu ya Aigupto, imene inali pa nyanja ya Firate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda.
3 Konzani cikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.
4 Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zacitsulo; tuulani nthungo zanu, bvalani malaya acitsulo.
5 Cifukwa canji ndaciona? aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osaceukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.
6 Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pa nyanja ya Firate wapunthwa nagwa.
7 Ndani uyu amene auka ngati Nile, madzi ace ogabvira monga nyanja?
8 Aigupto auka ngati Nile, madzi ace agabvira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ace.