7 Ndani uyu amene auka ngati Nile, madzi ace ogabvira monga nyanja?
8 Aigupto auka ngati Nile, madzi ace agabvira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ace.
9 Kwerani, inu akavalo; citani misala, inu magareta, aturuke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira cikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
10 Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza cilango, kuti abwezere cilango adani ace; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa nyanja ya Firate.
11 Kwera ku Gileadi, tenga bvunguti, namwali iwe mwana wa Aigupto; wacurukitsa mankhwala cabe; palibe kucira kwako.
12 Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kupfuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.
13 Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo adzafika adzakantha dziko la Aigupto.