1 Za Moabu Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Tsoka Nebo! pakuti wapasuka; Kiriyataimu wacitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lacitidwa manyazi lapasudwa.
2 Palibenso kutamanda Moabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu waanthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.
3 Mau amveka kucokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukuru!
4 Moabu waonongedwa; ang'ono ace amveketsa kulira.
5 Pakuti adzakwera pa cikweza ca Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa citsiko ca Horonaimu amva kulira kowawa kwa cionongeko.