12 Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zace, nadzaswa zipanda zao.
13 Ndipo Moabu adzacita manyazi cifukwa ca Kemosi, monga nyumba ya Israyeli inacita manyazi cifukwa ca Beteli amene anamkhulupirira,
14 Muti bwanji, Tiri amphamvu, olimba mtima ankhondo?
15 Moabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yace, ndi anyamata ace osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lace ndiye Yehova wa makamu.
16 Tsoka la Moabu layandikira kudza, nsautso yace ifulumiratu.
17 Inu nonse akumzungulira, mumcitire iye cisoni, inu nonse akudziwa dzina lace; muti, Cibonga colimba catyokatu, ndodo yokoma!
18 Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Moabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.