22 ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Beti-Dibilataimu;
23 ndi pa Kiriataimu, ndi pa Beti-Gamuli, ndi pa Beti-Meoni;
24 ndi pa Kerioti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Moabu, yakutari kapena yakufupi.
25 Nyanga ya Moabu yaduka, ndipo watyoka mkono wace, ati Yehova.
26 Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Moabu yemwe adzabvimvinika m'kusanza kwace, ndipo iye adzasekedwanso.
27 Kodi sunaseka Israyeli? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.
28 Inu okhala m'Moabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja cisanja cace pambali pakamwa pa dzenje.