38 Pamwamba pa macindwi a Moabu ndi m'miseu mwace muli kulira monse monse; pakuti ndaswa Moabu monga mbiya m'mene mulibe cikondwero, ati Yehova.
39 Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Moabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Comweco Moabu adzakhala coseketsa ndi coopsera onse omzungulira iye.
40 Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati ciombankhanga, adzamtambasulira Moabu mapiko ace.
41 Keroti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Moabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.
42 Ndipo Moabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, cifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.
43 Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, ziri pa iwe, wokhala m'Moabu, ati Yehova.
44 Ndipo iye wakuthawa cifukwa ca mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene aturuka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Moabu, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.