1 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israyeli alibe ana amuna? alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi cifukwa canji, ndi anthu ace akhala m'midzi mwace?
2 Cifukwa cace, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mpfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ace akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israyeli adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.
3 Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, mubvale ciguduli; citani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.
4 Cifukwa canji udzitamandira ndi zigwa, cigwa cako coyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira cuma cace, nati, Adza kwa ine ndani?
5 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akucokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ace, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osocera.