1 Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ace, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakucita zolungama, wakufuna coonadi; ndipo ndidzamkhululukira.
2 Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.
3 Yehova Inu, maso anu sali pacoonadi kodi? munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwa mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.
4 Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena ciweruzo ca Mulungu wao.
5 Ine ndidzanka kwa akuru, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi ciweruzo ca Mulungu wao. Koma awa anabvomerezana natyola gori, nadula zomangira zao.
6 Cifukwa cace mkango woturuka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene aturukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa ziri zambiri, ndi mabwerero ao acuruka.
7 Bwanji ndidzakhululukira iwe? pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anacita cigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama.