14 Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mpfuu.
15 Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yace, ndi luso anayala thambo;
16 pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, aturutsa mphepo ya m'nyumba za cuma zace.
17 Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golidi acitidwa manyazi ndi fanizo lace losema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya m'menemo.
18 Ngwacabe, ciphamaso; nthawi yakulangidwa kwao adzatayika.
19 Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndi mtundu wa colowa cace, dzina lace ndi Yehova wa makamu.
20 Iwe ndiwe cibonga canga ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzatyolatyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu;