16 Cifukwa cace iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mpfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.
17 Kodi suona iwe cimene acicita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu?
18 Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu yina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.
19 Kodi autsa mkwiyo wanga? ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?
20 Cifukwa cace, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.
21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.
22 Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera;