2 Ima m'cipata ca nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.
3 Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israyeli, Konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano.
4 Musakhulupirire mau onama, kuti, Kacisi wa Yehova, kacisi wa Yehova, kacisi wa Yehova ndi awa.
5 Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi macitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wace;
6 ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosacimwa m'malo muno, osatsata milungu yina ndi kudziipitsa nayo;
7 ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya,
8 Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.