25 Ciyambire tsiku limene makolo anu anaturuka m'dziko la Aigupto kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;
26 koma sanandimvera Ine, sanacherakhutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.
27 Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.
28 Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, coonadi catha, cadulidwa pakamwa pao.
29 Senga tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti se; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.
30 Pakuti ana a Yuda anacita coipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti alipitse.
31 Namanga akacisi a ku Tofeti, kuli m'cigwa ca mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao amuna ndi akazi; cimene sindinauza iwo, sicinalowa m'mtima mwanga.