1 Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!
2 Ha, ndikadakhala ndi cigono ca anthu aulendo m'cipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwacokere, pakuti onse ali acigololo msonkhano wa anthu aciwembu.
3 Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pacoonadi; pakuti alinkunkabe nacita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.
4 Mucenjere naye yense mnansi wace, musakhulupirire yense mbale wace; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.