3 Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pacoonadi; pakuti alinkunkabe nacita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.
4 Mucenjere naye yense mnansi wace, musakhulupirire yense mbale wace; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.
5 Ndipo yense adzanyenga mnansi wace, osanena coonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kucita zoipa.
6 Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.
7 Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzacitanji, cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu anga?
8 Lilime lao ndi mubvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wace pakamwa pace, koma m'mtima mwace amlalira.
9 Kodi sindidzawalanga cifukwa ca izi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu wotere?