2 Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wobvala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makara a moto ocokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndiri cipenyere ine.
3 Tsono akerubi anaima ku dzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzara bwalo la m'kati.
4 Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucokera kukerubi kumka ku ciundo ca nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi ceza ca ulemerero wa Yehova.
5 Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye.
6 Ndipo kunali pomlamulira munthu wobvala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga.
7 Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lace pakati pa akerubi ku moto uli pakati pa akerubi, naparako, nauika m'manja mwa iye wobvala bafuta, ndiye naulandita, naturuka.
8 Ndipo panaoneka pa akerubi conga dzanja la munthu pansi pa mapiko ao.