20 Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babulo, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwace anandilakwira nako.
21 Ndipo othawa ace onse m'magulu ace onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa ku mphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.
22 Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kulika; ndidzabudula nsonga yosomphoka'ya nthambi zace zanthete, ndi kuioka pa phiri lalitali lothubvuka;
23 pa phiri lothubvuka la Israyeli ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwace mudzakhala mbalame ziri zonse za mapiko ali onse; mu mthunzi wa nthambi zace zidzabindikira.
24 Ndipo mitengo yonse ya kuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kucicita.