7 Iwe tsono, wobadwa ndi munthu, ndakuika mlonda wa nyumba ya Israyeli, m'mwemo imva mau a pakamwa panga, nundicenjezere iwo.
8 Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumcenjeza woipayo aleke njira yace, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yace, koma mwazi wace ndidzaufunsa pa dzanja lako.
9 Koma ukacenjeza woipa za njira yace, aileke; koma iye osaileka njira yace, adzafa m'mphulupulu mwace iye, koma iwe walanditsa moyo wako.
10 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israyeli, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zocimwa zathu zitikhalira, ndipo ticita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?
11 Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yace, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?
12 Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu amtundu wako, Colungama ca wolungama sicidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwace, ndi kunena za coipa ca woipa, sadzagwa naco tsiku lakubwerera iye kuleka coipa cace; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi cilungamo cace tsiku lakucimwa iye.
13 Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama cilungamo cace, akacita cosalungama, sizikumbukika zolungama zace ziri zonse; koma m'cosalungama cace anacicita momwemo adzafa.