9 Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israyeli.
10 Koma Aleviwo anandicokera kumka kutariwo, posokera Israyeli, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.
11 Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira ku zipata za kacisi, ndi kutumikira m'kacisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera naime pamaso pao kuwatumikira.
12 Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala cokhumudwitsa ca mphulupulu ca nyumba ya Israyeli, cifukwa cace ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.
13 Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira nchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga ziri zonse zopatulikitsazo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazicita.
14 Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa kacisi kwa utumiki wace wonse, ndi zonse zakumacitika m'mwemo.
15 Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israyeli, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;