16 Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndiye mtundu wa colowa cace; dzina lace ndi Yehova wa makamu.
17 Nyamula katundu wako, iwe wokhala m'linga.
18 Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.
19 Tsoka ine, ndalaswa! bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu bvuto langa ndi ili, ndipirire nalo.
20 Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga aturuka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kucinga nsaru zanga,
21 Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; cifukwa cace sanapindula; zoweta zao zonse zabalalika.
22 Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikuru lituruka m'dziko la kumpoto, likacititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe.