7 Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawaturutsa iwo ku dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.
8 Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.
9 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ciwembu caoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu.
10 Abwerera kucitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu yina kuti aitumikire; nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.
11 Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo coipa, cimene sangathe kucipulumuka; ndipo adzandipfuulira Ine, koma sindidzamvera iwo.
12 Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzapfuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.
13 Pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira camanyazi, alingana ndi kucuruka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.