8 Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
9 Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.
10 Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.
11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.
12 Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.
13 Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.
14 Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao.