11 Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi yansautso.
12 Kodi angathe munthu kutyola citsulo, citsulo ca kumpoto, ndi mkuwa?
13 Cuma cako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wace, icico cidzakugwera cifukwa ca zocimwa zako zonse, m'malire ako onse.
14 Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako ku dziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.
15 Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire ine, mundibwezere cilango pa ondisautsa ine; musandicotse m'cipiriro canu; dziwani kuti cifukwa ca Inu ndanyozedwa.
16 Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine cikondwero ndi cisangalalo ca mtima wanga; pakuti ndachedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.
17 Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekera-sekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha cifukwa ca dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.