17 Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la coipa.
18 Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la coipa, muwaononge ndi cionongeko cowirikiza.
19 Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'cipata ca ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene aturukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu;
20 ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala m'Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi;
21 atero Yehova: Tadziyang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;
22 musaturutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire nchito iri onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;
23 koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve, asalandire langizo.