19 Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'cipata ca ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene aturukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu;
20 ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala m'Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi;
21 atero Yehova: Tadziyang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;
22 musaturutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire nchito iri onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;
23 koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve, asalandire langizo.
24 Ndipo padzakhala, ngati mu ndimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira nchito m'menemo;
25 pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akuru okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera pa magareta ndi akavalo, iwo, ndi akuru ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala ku nthawi zamuyaya.