4 Iwe, iwe wekha, udzaleka pa colowa cako cimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha ku nthawi zamuyaya.
5 Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nucoka kwa Yehova mtima wace.
6 Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'cipululu, ndipo saona pamene cifika cabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'cipululu, dziko lacikungu lopanda anthu.
7 Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene cikhulupiriro cace ndi Yehova.
8 Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.
9 Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosaciritsika, ndani angathe kuudziwa?
10 Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zace, monga zipatso za nchito zace.