11 Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.
12 Cifukwa cace njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzacotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.
13 Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasokeretsa anthu anga Israyeli.
14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona cinthu coopsetsa; acita cigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ocita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zace; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ace ngati Gomora.
15 Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.
16 Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zacabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.
17 Anena cinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wace amati, Palibe coipa cidzagwera inu.